Press Release

TSIKU LOKUMBUKIRA NTCHITO YOLIMBANA NDI ZIPHUPHU PA DZIKO LONSE LA PANSI

TSIKU LOKUMBUKIRA NTCHITO YOLIMBANA NDI ZIPHUPHU PA DZIKO LONSE LA PANSI

CHIDZIWITSO

9 December ndi tsiku lokumbukira ntchito yolimbana ndi mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale pa dziko lonse. Tsikuli linakhazikitsidwa pamsonkhano wa maiko a United Nations m’chaka cha 2003.

Chaka chino ku Malawi kuno, tsikuli likumbukiridwa pa mutu wakuti “Tithetse Ziphuphu: Adindo Afotoze Ntchito Zawo”. Mutuwu ukutilimbikitsa tonse kutenga mbali polimbana ndi ziphuphu. Adindo akuyenera kufotokozera anthu amene amawatumikira momwe iwo akugwilira ntchito zawo komanso anthu akuyenera kutenga mbali pofunsa adindo kuti alongosole momwe iwo akugwilira ntchito zawo pamene akuwatumukira. Izi zidzathandiza kupititsa patsogolo ntchito zosiyanasiyana zotukula miyoyo ya anthu m’dziko muno.

 Bungwe la Anti-Corruption Bureau likudziwitsa nonse kuti mwambo wokumbukira ntchito yolimbana ndi ziphuphu pa dziko lonse chaka chino udzachitika loweruka pa 9 December, 2017 ku Bingu International Convention Center (BICC), ku Lilongwe kuyambira nthawi ya 9 koloko m’mawa.

 Cholinga chokumbukira tsikuli ndikufuna kuzindikilitsa anthu onse m’Malawi muno kuipa kwa m’chitidwe wa ziphuphu ndi kupeza njira zabwino zothandiza kuteteza kuti mchitidwewu usapitilire kuononga dziko lathu.

Pa tsikuli kudzakhala zokambirana zotsogozedwa ndi akuluakulu a ku ofesi ya Mkulu Ozenga Milandu (DPP), Ofesi ya Mkulu Oyang’anira zakagulidwe kabwino kakatundu wa boma (ODPP),  Bungwe lothetsa ziphuphu ndi katangale (ACB), ndi wapampando wa bungwe la atolankhani la NAMISA.  Katswiri wa ndakatulo, Robert Chiwamba adzalakatulanso ndakatulo zogwirizana ndi mutu wa tsikuli. Zochitikazi zidzaulutsidwa pa wailesi ya Zodiak (ZBS). Bungwe la Anti-Corruption Bureau likupempha a Malawi onse kuti adzamvere ndi kutenga nawo mbali pa zochitika za tsikuli kudzera pa wailesiyi.

Tiyeni tithetse ziphuphu pofotokoza zomwe tikuchita ngati adindo ndikufunsa adindo kufotokoza pa ntchito zawo.

 

 

REYNECK MATEMBA

ACTING DIRECTOR-GENERAL

Posted on