Press Release

KUSAMUKA KWA OFESI ZA ACB KUCHOKA KU MA OFESI A NATIONAL BANK OF MALAWI KUPITA KU NYUMBA YA ABLE

KUSAMUKA KWA OFESI ZA ACB KUCHOKA KU MA OFESI A NATIONAL BANK OF MALAWI KUPITA KU NYUMBA YA ABLE

Bungwe la Anti-Corruption Bureau likudziwitsa anthu onse kuti ma ofesi ake a ku Blantyre asamutsidwa kuchoka mu nyumba yomwe inali likulu lakale la National Bank kupita ku nyumba ya Able pa plot nambala BW180 m’mbali mwa msewu wa Hannover. Maofesiwa ali pafupi ndi sukulu ya Zokopa alendo ya Malawi Institute of Tourism.

Bungwe la ACB likutsimikizira anthu onse kuti lipitilira kugwira ntchito zake zonse ku maofesi ake atsopanowa. Adiresi ndi manambala a lamya sadasinthe.

Bungweli likupepesa onse chifukwa cha zovuta zomwe anakumane nazo kaamba ka kusamukaku.

REYNECK MATEMBA
DIRECTOR GENERAL